Featured Posts
KUKANA NSALU YA AKULU NKUBVIIKA
- Get link
- X
- Other Apps
KUKANA NSALU YA AKULU NKUBVIIKA
Akulu akanena mau amene sukhutira, m'malo mwakukana kwamanyazi ukana mwakuzembetsa kuti mkuluyo asachite manyazi.
Afanizira nsalu monga mkulu anamtuma mwana kuti akachape ndipo sanafune kupita, koma poona kuti angamuchititse manyazi mkuluyo, anangopita nangobviika nabwera nayo.
Mkuluyo anadziwa kuti mwanayo anangolola chifukwa chamanyazi.
Pogwira nchito nchimodzi-modzi, m'malo mwakukaniratu koma kuchita pang'ono.
Poweruza mlandu nchimodzi-modzi ngati akulu anena mau amene sangakhale otheka kweni-kweni, pofuna kukana akulu amanena mau amenewa,
"Mwanawe, kayese choncho. Kukana nsalu ya akulu nkubviika."
_______________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment