Featured Posts
MLENDO NDI AMENE AYENDA NDI KALUMO KAKUTHWA
- Get link
- X
- Other Apps
MLENDO NDI AMENE AYENDA NDI KALUMO KAKUTHWA
Ponena mlandu pamakhalapo ena omvera mlanduwo ena amakhala odzera kwina kutali.
Mwina oweruza angaponyere mlandu kwa alendo kuti, "Tatithandizani pamenepo kuweruza kwache."
Iye amakana nati, "Ine ndine mlendo, sindingadziwe kuweruza."
Atatero mpamene pamadzera mau amenewa kuti, "Ngakhale mlendo angaweruze kupambana eni ache popeza nayenso kwao amakhala pabwalo la mirandu."
Pochula kalumo ndi kuti:
*Kale-kale pamudzi wina analikumeta maliro, ndipo popeza anali anthu ambiri lumo lache linabuntha.
Pompo panafika mlendo ali ndi thumba lache. Iye poona kuti anthu analikusauka anati,
"Tabwerekani kalumo kangaka muyese."
Poyesa anaona kuti kanali kakuthwa kupambana ndi lao lija, kotero anatha kumetera onse.
Mwinanso mlendo angamve zambiri za iwe za chiwembu, angakuuze kumene kuchokera chaupandu, popeza akamanena za iwe samasamala ngati pali mlendo pafupi, chifukwa adziwa kuti alibe nazo kanthu.
_____________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment