Featured Posts
GALU WA MKOTA SAKANDIRA PACHABE
- Get link
- X
- Other Apps
GALU WA MKOTA SAKANDIRA PACHABE
Ponena mlandu kapena nkhani anthu akamatsutsana, koma ena nangolimbikira mwa khama, ena anzeru pakumva amaponya mwambi umenewu.
Pamenepo nzeru yake ndi kuti, galu amene wazolowera kusaka nakula nakhala ndi ana samakandira pa dzenje popanda kanthu monga amachita agalu oyamba kuphunzira kusaka m'thengo. Wamkota amakandira pamene pali kanthu, nyama kapena mbewa.
Agalu ena aang'ono amangokandira mwa masewera ngakhale popanda kanthu.
Koma wamkota akamakandira, ngakhale agalu ena a ang'ono asasamale, anthu amadziwa kuti pamenepo pali kanthu, ndipo poyesa kukumba amapeza patuluka kanyama kapena mbewa.
Nchifukwa chache amafanizira akulu amene anaona zinthu zamitundu-mitundu za m'dziko, odziwa kuweruza mirandu, ndi kuyesa kudziwa zinsinsi ndi zomwe zingaonekere mtsogolo.
Enawo ndiwo agalu ophunzira kusaka-kuphunzira kuweruza.
Mau awa amanenedwanso mwina za munthu amene amakakamira pa chinthu kapena kuchizolowera ndipo ngakhale zobisika poyamba, nthawi zina chimaululidwa mtsogolo mwake.
KONKHANI MIYAMBI YINA MUSIMU
______________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment