Featured Posts
KANDIMVERERE ANANENA ZA M'MALUWA
- Get link
- X
- Other Apps
KANDIMVERERE ANANENA ZA M'MALUWA
Maka-maka mwambi uwu umanenedwa kwa Mboni yonama imene sinamvetse za mlandu machitidwe ache, penanso kwa munthu wosadziwa ndi wosafunsa, kapena amene amakonda kutuma anzake kuti,
"Tapitani mundimverere mauwo mudzandiuze mukabwera."
Iye sakonda kupita kukaona ndi kuphunzira ndi anzake m'mene anakambira nkhani.
Nthano yache ndiyo:
*Panali munthu ndi mphwache(Nephew). Mkuluyo anali wodziwa kufula njuchi, koma wamng'onoyo analikungodya wosafunsa ndiponso wosatsagana naye mkulu wake kukafula njuchi.
Popita nthawi mkulu wache anatopa kumgawira namangodya yekha.
Tsiku lina mphwa wakeyo anapita m'thengo kukafuna njuchi ndipo anazipeza zirikuuluka-uluka m'maluwa.
Popeza sanadziwa polowera pa njuchi, iye ananena mwa yekha nati, "Lero nane ndazipeza zanga, ndikauza mkulu wanga adzandithandize kufula."
Iye anabwerera kumudzi nakauza mkulu wache nati,
"Akulu anga ndaona njuchi zanga zabasi, tiyeni mukandithandize kufula."
Mkulu wake anamfunsitsa, "Wazionadi?"
Nati, "Inde zambiri-mbiri."
Nati, "Chabwino tenga nsompho, maudzu ndi moto, tiye tsogola njira."
Iwo atafika pamalopo anapeza pali zii! Mkuluyo nafunsa,
"Nanga ziri kuti?"
Mphwache nati, "Zimauluka pamaluwa ponsepa." Mkuluyo anadziwa kuti zinalikutenga Uchi m'maluwa nati, "Zimenezo nzamaluwa (zotenga Uchi), si njuchi zeni-zeni."
Nchimodzi-modzi kutenga nkhani za m'kamwa-m'kamwa, osati zeni-zeni.
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
________________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment