Featured Posts
KHOSWE AKAKHALA PA MKHATE SAPHEKA
- Get link
- X
- Other Apps
KHOSWE AKAKHALA PA MKHATE SAPHEKA
Tanthauzo la mwambi uwu ndilo kuti khoswe akakhala pa mkhate chifuniro chimafika kuti umuphe, koma umalingaliranso za mkhate wako kuti, "Ndikammenya ndi ndodo kapena ndi mwala, ndiswa mkhate wanga wopambana ndi khoswe."
Chifukwa cha chimenechi ungomuthamangitsa.
Momwemo pakuweruza mlandu wa mkulu wako atachimwira ena, pamakhala pobvuta kwambiri.
Nchimodzi-modzinso kanthu kakakuonekera mwadzidzidzi kapena pafupi, sikamachitika bwino.
Uwu ndi mwambi umene oweruza amanena, akaona kuti mlanduwo uli wamwanansi(bululu) wake, kuti ena aweruze m'malo mwa iwo. Wina wofanana ndi womwewo ndi uwu:
Mbalame ikakhala pa uta sirasika
Afanizira munthu wosaka mbalame, watenga uta m'manja, mbalame yabwera ndi kutera pa uta, iye ngakhale amasaka mbalame angasowe nzeru yochita.
Ndipo ngakhale akhale mmisiri woponya kotani alephera kuirasa.
Chomwecho ndi mlandu adzalephera kuweruza, wamgwera m'manja mwake.
KONKHANI MIYAMBI YINA MUSIMU
_____________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment