Featured Posts

Download BlueEye Lite the Social Media designed for you

Image
DOWNLOAD BLUEEYE LITE — THE SOCIAL PLATFORM DESIGNED FOR YOU 🌍  BlueEye Lite  is not just another app—it’s a bold, inclusive social media platform built to empower creators, connect communities, and give every user a voice. Whether you're posting, reacting, or discovering new content,  BluEye Lite  is designed to feel natural, secure, and universally accessible. 🛠️  Crafted and branded by Dr. Mtonga N. Isaac , a visionary platform architect based in Lusaka, Zambia,  BlueEye Lite  reflects a deep commitment to privacy, clarity, and real-world usability. Every feature is built with purpose—from secure onboarding to expressive media sharing. ✨ What makes  BlueEye Lite  stand out: ✅  Clean, responsive design  for mobile friendly ✅  Secure login  with phone or email—your data stays yours ✅  Open posting  with reactions, replies, and media previews ✅  Modular features  that evolve with your needs 📢  Y...

KUNENA KWA NDITHE-NDITHE NAMUNTHAMBWE ANAZITENGERA


KUNENA KWA NDITHE-NDITHE NAMUNTHAMBWE ANAZITENGERA

Mwambi wakuletsa kuyankhira nkhani za eni ache.

Akulu ponena mlandu amakonda kwambiri kuphiphiritsa nkhani zao, ndipo wina akaulula chinsinsi chao amamlekera kuti aweruze ndiye. 

Iwo amangofuna kuti akaphiphiritse pakuona kuchita manyazi akumvawo kapena kuti oweruzidwawo azindikire okha nasiye chimene awatsutsacho.

Mwambiwu uli ndi nthano yache ndiyo:

 *Kale-kale namnthambwe, timba ndi mbalame zina zinali zakupha nyama ndi maukonde ao. Namnthambwe, timba ndi mbalame zina zinali zodikira maukonde. 

Mwa mbalame zonse woponya uta kwambiri anali timba; akaponya mubvi wache wosagwera m'dothi. Masiku onse namnthambwe analikukhalira ukonde umodzi ndi timba. 

Iwo onse atapita ku uzimba, mbalame zina zinanka kukasaka ndipo inabvumbuluka nyama nikodwa mu ukonde wa namnthambwe ndi timba. Timba anaponya mubvi nairasa nati mau apansi, "Atate!"

 Pakumva namnthambwe anapfuula ndi mau okweza (adziti walasa ndiye)

"Namnthambwe! Namnthambwe! Namnthambwe!"

Pakumva mbalame zina zinakhulupirira kuti ndiye walasa, pofika kufunsa zapeza nyama iri gone! 

Timba kulephera kunenetsa kuti ndalasa ndine, koma mbalamezo zinati, "Ife tamva dzina la Namnthambwe si Timba ai."

Machitidwe oterewa anachitidwa pa uzimba uliwonse, koma Timba sanamve bwino m'mtima mwache nayesa-yesa njira yakumuletsera Namnthambwe mkhalidwe woterewo.

Tsiku lina anapanga malango kuti Namnthambwe atenge mlandu. Mbalame zonse zitapangana kunka kuuzimba Namnthambwe ndi Timba anakhalira ukonde umodzi monga mwa masiku onse. 

Tsiku limenelo nyama itabvumbuluka Timba m'malo molasa nyama, analasa mmodzi wa odikira nati chimodzi-modzi mau apansi monga mwamasiku onse, "Atate!" 

Namnthambwe pakumva anachita mwa masiku onse napfuula,

"Namnthambwe! Namnthambwe! Namnthambwe!"

Zitabwera mbalame zonse zinati, "Kodi nyama imene unkanenererayo ndi imeneyi?" 

Iye analephera kukana nayesa kutulira mlanduwo pa Timba koma izo zinachitira umboni ndi kuti, "Walasa mnzathu ndiwe chifukwa tamva mau ako." 

Pompo zinamgwira ndi kumupha.

*Mwambi umenewu ukumbutsa kuti anthu ambiri amalowa m'zobvuta chifukwa chakuulula-ulula zinsinsi zaeni, natengedwa pa mlandu, mwina kulangidwa opanda kuchimwa koma chifukwa cha mau okha, monga namnthambwe uja.

KONKHANI MIYAMBI YINA MUSIMU

www.miyambi.com

________________________________________________________________

Contact us:


Mtonga Isaac Pharmacy,

Ng'ombe Township,

#16/24 Off Zambezi road,

Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,

Tel: +260974272433/+260966399444,

Lusaka, Zambia .

Comments

Popular Posts

CERVICAL STENOSIS(BLOCKED CERVIX) AND TREATMENT

ERECTILE DYSFUNCTION (IMPOTENCE) AND TREATMENT

PELVIC INFLAMMATION DISEASE (PID) AND TREATMENT

MISCARRIAGE (PREGNANCY LOSE) AND TREATMENT

AMENORRHEA AND TREATMENT

TWIN PREGNANCY AND GUIDELINES

ENDOMETRIOSIS AND TREATMENT