Featured Posts
LERO LOMWE LINADETSA MNTHENGU
- Get link
- X
- Other Apps
LERO LOMWE LINADETSA MNTHENGU
Nthano yache ndi iyi:
Panali mnyamata wobiriwira bwino amene pobvina chamba akazi analikumkonda kwambiri chifukwa cha kubiriwira kwache.
Chotero mnthengu anamfunsa mnyamata nati, "Kodi kubiriwira kotereku unakutenga bwanji kuti akukonde akazi chotere?"
Iye anati, "Kwa munthu ali pamudzipo, ukafuna pita pomwepo."
Mnthengu anapita nampeza mwini mankhwala aja obiriwiritsa thupi.
Mwini mankhwalayo anati, "Mwachedwa atha ndithu."
Koma mnthengu anaumirira kuti, "Ai patseni, ndapota nanu."
Wamankhwalayo anati, "Chabwino kabwere mawa."
Mnthengu anakana nati, "Ai, ndifuna lero lomwe."
Mwini mankhwalayo anangotenga nsupa ya mafuta osanganiza ndi makala kungomkhuthulira m'thupi monse.
Ndicho chifukwa chache mnthengu ali wakuda.
Tikafuna chinthu tisamati, "Lero lomwe ai," tidziyamba taganizira.
Pa mlandu nchimodzi-modzi, chifukwa oweruza akatopa angaweruze moipa.
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
__________________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment