Featured Posts
PATSALA PAJA PAGONA CHINZIRI
- Get link
- X
- Other Apps
PATSALA PAJA PAGONA CHINZIRI
Mwambi uwu umatsutsa munthu amene amanenanena zakale zothaitha. Mwina akamabwereza-bwereza mau onena-nena kale ndiponso kukumbutsa mlandu wotha kale.
Mau a mwambi uwu kumasulira kwache ndiko:
*Munthu akalima munda wache watsopano (mphanje),. sumakhala wowirira kwambiri.
Nthawi yina ukaguga, amausiya ndi kukhala thengo limene timalicha Tsala, ndipo pamatsala pamakonda zinziri (Quail) ndi kuikira mazira ndi kuswa ana ndi kumakhala pompo.
Tanthauzo lache licokera pamenepo popeza mposiya-siya posalima, palibe kanthu. Choncho munthu sanganene kuti munda koma tsala.
Nchimodzi-modzi ndi munthu wonenanena nkhani yakalekale yothaitha kuyesa kukometsera mlandu wache womgwera. Woteroyo ndi amene amamunenera mwambi umenewu.
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
________________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/++260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment