Featured Posts
PAWIRI SIPAUZIRIKA
- Get link
- X
- Other Apps
PAWIRI SIPAUZIRIKA
Mwambi woletsa kusanganiza nkhani pa mlandu ngati munthu anena mau awiri amapatsa kukayikitsa oweruza mlanduwo.
Mwambi umenewu tanthauzo lache linachokera pa munthu pakukumba mbewa, atapeza kuti zalowa m'mauna awiri ndipo afuna kuuzirira mauna onsewo yekha.
Pakuyesa aona kulephera kwache. Ichi ndi chifukwa chache akulu ananena mwambiwo poona kuti mirandu iwiri kuilowetsa mu mlandu umodzi zimakhala zobvuta, sangathe kuweruza pamodzi.
Mwambiwu unganenedwe pophunzitsa chikhalidwe cha mtima kuti munthu amene amafuna zinthu zambiri pa nthawi imodzi adzalephera.
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
_______________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia .
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment