Featured Posts

Chat Platform

Image
HealthChat Feed Create a Post Post

NZERU-NZAYEKHA ANABVIIKA NSIMA M'MANZI


NZERU-NZAYEKHA ANABVIIKA NSIMA M'MANZI

Kuyerekezera munthu amene akana zolangizidwa ndi anthu. Sumanenedwa pa mlandu pokha komanso ngakhale pakukambirana kapena pakuphunzitsa ana. 

Nthano ya mwambi umenewu ndiyi:

*Kale-kale panali munthu dzina lache Nzeru-nzayekha, ndiko kusafuna kumulangiza anzake. Anzake anayesa-yesa kumulangiza njira ndi njira chomwe amachita poyenda anthu kunja kuno, koma iye kulephereka.

Tsiku lina iye analikumanga nyumba ndi anzache. Iwo anamuyesa aone ngati angathe kudziwa zobisika. 

Anatenga nsima pamodzi ndi Ndiwo zake namanga m'maluzi ndipo anamtuma kukabviika maluziwo. Iye anangopita mosadziwa nakabviika m'madzi nabwera. 

Anzake anamfunsa, "Kodi nsima ija mwadya, Che Nzeru-nzayekha?" 

Iye anafunsa, "Iri kuti?" 

Iwo nati, "Kodi simunaione m'maluzi muja?" 

Iye anati, "Kodi chifukwa chiani osandiuza poyamba pomwe kuti munamanga nsima?" 

Iwo anati, "Iwe ndiwe Nzerunzayekha wod-

ziwa wekha zonse." 

Iye popita kumadzi kukabvuula maluzi, anangoona nsima yonyenyeka irikuyanda-yanda pamadzi ndi Ndiwo zomwe. 

Poona zoterezi anasintha dzina lache nati, "Ine dzina langa tsopano ndine 'Nzeru-nkupangwa', amene alandira malangizo kwa anzache.

" Tsopano makhalidwe ake onse anasinthika chifukwa cha dzinalo. 

Pali miyambi yina yofanana ndi umenewu monga:

Safunsa anadya Phula

KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA

www.mtongaisaacpharmacy.com

_________________________________________________________________

Contact us:


Mtonga Isaac Pharmacy,

Ng'ombe Township,

#16/24 Off Zambezi road,

Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,

Tel: +260974272433/+260966399444,

Lusaka, Zambia .


_______________________________________
_______________________________________
________________________________________

Mtonga Isaac Pharmacy Zambia

NAME & SURNAME:
EMAIL ADDRESS
MESSAGE:
_______________________________________

Comments

Popular Posts

CERVICAL STENOSIS(BLOCKED CERVIX) AND TREATMENT

ERECTILE DYSFUNCTION (IMPOTENCE) AND TREATMENT

PELVIC INFLAMMATION DISEASE (PID) AND TREATMENT

AMENORRHEA AND TREATMENT

ENDOMETRIOSIS AND TREATMENT

MISCARRIAGE (PREGNANCY LOSE) AND TREATMENT

CD4 - CD8 COUNT AND TREATMENT