Featured Posts
SAFUNSA ANADYA PHULA
- Get link
- X
- Other Apps
SAFUNSA ANADYA PHULA
Alipo anthu amene amangokwiyira anzao pa chifukwa chosadziwika. Kuteroko nchimodzi-modzi kudya phula.
Nthano ya mwambi umenewu ndi iyi:
*Kale-kale panali munthu dzina lache Safunsa. Iye anali kumva anzache namanena-nena za zinthu zina ndi zina, koma iye wosafunsa.
Mwina anzache akaona njuchi zirikuyenda kufuna maluwa ndi kuyamba kukambiirana.
"Taonani njuchi zitenga madzi (uchi), ndiganiza tsopano zaika. Utazipeza ziri phula nyati, uzifula ndi kuzidya."
Safunsa zonsezi kumangomvera wosafunsa kumene amapeza phula kapena mafulidwe ache.
Tsiku lina iye anapita m'thengo kukafuna njuchi. Mwamwai anazipeza, phula liri umbirire polowera. Iye pompo chimwemwe wayamba kusekera nati, "Lero ndazipeza njuci zija amanena anzanga, ndizidya."
Pompo iye anayamba kudya phulalo koma sanamve kukoma, linangokakamiranso m'miromo mwache.
Iye poona zoterezi anatenga phula lapang'ono nasiya dzina lache ku thengo (ndiko kuti iye anayamba kuganiza zakufunsa kumudzi amene anali wosafunsa kale) nafika kumudzi nafunsa,
"Kodi njuchi amadya zokoma zija ndi zimenezi ndatengazi, zoumitsa m'miromo?"
Kuyankha kwa anzache anati,
"Kodi unalekeranji kufunsa? Si phula limenelo lija amata pa ng'oma? Njuchi zimakhala mkati."
Iye tsopano anasanduka dzina lache Mfunsi.
Mwambi wina wofanana ndiwo:
Kandimverere ananena za m'maluwa
KONKHANI MIYAMBI YINA PASIPA
_________________________________________________________________
Contact us:
Mtonga Isaac Pharmacy,
Ng'ombe Township,
#16/24 Off Zambezi road,
Email: mtongaisaacpharmacy@gmail.com,
Tel: +260974272433/+260966399444,
Lusaka, Zambia.
_______________________________________ _______________________________________
Comments
Post a Comment